Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa, achititse kuti nkhope yake itiwalire.Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe, pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.Nthaka yabereka zokolola zake; tidalitseni Mulungu wathu.Mulungu atidalitse kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.