1Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake. 2Udzadya chipatso cha ntchito yako; madalitso ndi chuma zidzakhala zako. 3Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka mʼkati mwa nyumba yako; ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi kuzungulira tebulo lako. 4Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa amene amaopa Yehova. 5Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni masiku onse a moyo wako; uwone zokoma za Yerusalemu, 6ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israeli.