Masalimo 67

Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa, achititse kuti nkhope yake itiwalire. Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse. Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni. Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe, pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi. Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni. Nthaka yabereka zokolola zake; tidalitseni Mulungu wathu. Mulungu atidalitse kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

Unseren Newsletter abonnieren

Bleiben Sie über neue Profile, Veranstaltungen und Plattform-Updates informiert.