1Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu; onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu. 2Imvani pemphero langa, Inu Mulungu mvetserani mawu a pakamwa panga. 3Alendo akundithira nkhondo; anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga, anthu amene salabadira za Mulungu. 4Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa; Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine. 5Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe; mwa kukhulupirika kwanu awonongeni. 6Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu; ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova, pakuti ndi labwino. 7Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse, ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.