Masalimo 150

Tamandani Yehova. Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika; mutamandeni ku thambo lake lamphamvu. Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu; mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana. Mutamandeni poyimba malipenga, mutamandeni ndi pangwe ndi zeze. Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina, mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro. Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga, mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri. Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova. Tamandani Yehova.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

订阅我们的新闻通讯

及时了解新的资料页、活动与平台更新。