Masalimo 3

Inu Yehova, achulukadi adani anga! Achulukadi amene andiwukira! Ambiri akunena za ine kuti, “Mulungu sadzamupulumutsa.” Sela Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza, Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula. Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. Sela Ine ndimagona ndi kupeza tulo; ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza. Sindidzaopa adani anga osawerengeka amene abwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse. Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa. Chipulumutso chimachokera kwa Yehova. Madalitso akhale pa anthu anu. Sela

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

订阅我们的新闻通讯

及时了解新的资料页、活动与平台更新。