Masalimo 126

Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni, tinali ngati amene akulota. Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka; malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe. Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti, “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.” Yehova watichitira zinthu zazikulu, ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe. Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova, monga mitsinje ya ku Negevi. Iwo amene amafesa akulira, adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe. Iye amene amayendayenda nalira, atanyamula mbewu yokafesa, adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe, atanyamula mitolo yake.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

订阅我们的新闻通讯

及时了解新的资料页、活动与平台更新。