Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima.Israeli asangalale mwa mlengi wake; anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo.Atamande dzina lake povina ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe.Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake; Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa.Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo, ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo,kubwezera chilango anthu a mitundu ina, ndi kulanga anthu a mitundu yonse,kumanga mafumu awo ndi zingwe, anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo,kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse. Tamandani Yehova.