Masalimo 131

Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza, maso anga siwonyada; sinditengeteka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa. Koma moyo wanga ndawutontholetsa ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa, moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa. Yembekeza Yehova, iwe Israeli, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

订阅我们的新闻通讯

及时了解新的资料页、活动与平台更新。