Masalimo 138

Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse; ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.” Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera ndipo ndidzayamika dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu, pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu kupambana zinthu zonse. Pamene ndinayitana, munandiyankha; munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima. Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova, pamene amva mawu a pakamwa panu. Iwo ayimbe za njira za Yehova, pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu. Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa, koma anthu onyada amawadziwira chapatali. Ngakhale ndiyende pakati pa masautso, mumasunga moyo wanga; mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga, mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja. Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine; chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha musasiye ntchito ya manja anu.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

订阅我们的新闻通讯

及时了解新的资料页、活动与平台更新。