Masalimo 149

Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima. Israeli asangalale mwa mlengi wake; anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo. Atamande dzina lake povina ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe. Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake; Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa. Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo. Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo, ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo, kubwezera chilango anthu a mitundu ina, ndi kulanga anthu a mitundu yonse, kumanga mafumu awo ndi zingwe, anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo, kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse. Tamandani Yehova.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

Subskrybuj nasz newsletter

Bądź na bieżąco z nowymi profilami, wydarzeniami i nowościami platformy.