1Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, anene tsono Israeli, 2akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, potiwukira anthuwo, 3iwo atatipsera mtima, akanatimeza amoyo; 4chigumula chikanatimiza, mtsinje ukanatikokolola, 5madzi a mkokomo akanatikokolola. 6Atamandike Yehova, amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo. 7Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame yokodwa mu msampha wa mlenje; msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka. 8Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.