“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” anene tsono Israeli;“Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, koma sanandipambane.Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali:Koma Yehova ndi wolungama; Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.”Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi.Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule;sungadzaze manja a owumweta kapena manja a omanga mitolo.Odutsa pafupi asanene kuti, “Dalitso la Yehova lili pa inu; tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”