Inu Mulungu musakhale chete; musangoti phee, Mulungu musangoti duu.Onani adani anu akuchita chiwawa, amene amadana nanu autsa mitu yawo.Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu; Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda.Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu kuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.”Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu; Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu:Matenti a Edomu ndi Aismaeli, Mowabu ndi Ahagiri,Agebala, Aamoni ndi Aamaleki, Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo kupereka mphamvu kwa ana a Loti. SelaMuwachitire zomwe munachitira Amidiyani, monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni.Amene anawonongedwa ku Endori ndi kukhala ngati zinyalala.Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebu ana a mafumu muwachite zomwe munachita Zeba ndi Zalimuna,amene anati, “Tiyeni tilande dziko la msipu la Mulungu.”Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga, ngati mankhusu owuluka ndi mphepo.Monga moto umatentha nkhalango, kapena malawi a moto kuyatsa phiri,kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho, ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe.Muphimbe nkhope zawo ndi manyazi kuti adzafunefune dzina lanu Yehova.Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse; awonongeke mwa manyazi.Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova, ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.