Imbirani Yehova nyimbo yatsopano; Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.Imbirani Yehova, tamandani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda; ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano, koma Yehova analenga mayiko akumwamba.Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake, mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake; bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake; njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.” Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe; Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere; nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo. Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe;idzayimba pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lonse mwachilungamo ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.