1Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu? Akonzekeranji zopanda pake anthu? 2Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo. 3Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo ndipo titaye zingwe zawo.” 4Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo. 5Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti, 6“Ine ndakhazikitsa mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.” 7Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula: Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga; lero Ine ndakhala Atate ako. 8Tandipempha, ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako; malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako. 9Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo; udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.” 10Kotero, inu mafumu, chenjerani; chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi. 11Tumikirani Yehova mwa mantha ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera. 12Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.