Masalimo 124

Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, anene tsono Israeli, akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, potiwukira anthuwo, iwo atatipsera mtima, akanatimeza amoyo; chigumula chikanatimiza, mtsinje ukanatikokolola, madzi a mkokomo akanatikokolola. Atamandike Yehova, amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo. Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame yokodwa mu msampha wa mlenje; msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka. Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

Abonner på nyhetsbrevet vårt

Hold deg oppdatert på nye profiler, arrangementer og plattformnyheter.