Ombani mʼmanja, inu anthu onse; fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba; Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu; anayika anthu pansi pa mapazi athu.Iye anatisankhira cholowa chathu, chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda. SelaMulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe, Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando; imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani Iye salimo la matamando.Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana monga anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu; Iye wakwezedwa kwakukulu.