1Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu; Iye akuweruza pakati pa “milungu.” 2“Mudzateteza osalungama mpaka liti, ndi kukondera anthu oyipa? 3Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika. 4Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa. 5“Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse. Amayendayenda mu mdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. 6“Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu, nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’ 7Koma mudzafa ngati anthu wamba; mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.” 8Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi, pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.