Mwa Yehova ine ndimathawiramo. Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti, “Thawira ku phiri lako ngati mbalame.Pakuti taona oyipa akunga mauta awo; ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta, pobisala pawo kuti alase olungama mtima.Tsono ngati maziko awonongeka, olungama angachite chiyani?”Yehova ali mʼNyumba yake yoyera; Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba. Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu; maso ake amawayesa.Yehova amayesa olungama, koma moyo wake umadana ndi oyipa, amene amakonda zachiwawa.Iye adzakhuthulira pa oyipa makala amoto ndi sulufule woyaka; mphepo yotentha idzakhala yowayenera.Pakuti Yehova ndi wolungama, Iye amakonda chilungamo; ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.