Masalimo 133

Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano! Zili ngati mafuta amtengowapatali othiridwa pa mutu, otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aaroni, oyenderera mpaka mʼkhosi mwa mkanjo wake. Zili ngati mame a ku Heremoni otsikira pa Phiri la Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso, ndiwo moyo wamuyaya.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

뉴스레터 구독

새로운 프로필과 행사, 플랫폼 소식을 받아 보세요.