Masalimo 123

Ndikweza maso anga kwa Inu, kwa Inu amene mumakhala kumwamba. Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo, monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake, choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu, mpaka atichitire chifundo. Mutichitire chifundo, Inu Yehova mutichitire chifundo, pakuti tapirira chitonzo chachikulu. Ife tapirira mnyozo wambiri kuchokera kwa anthu odzikuza, chitonzo chachikulu kuchokera kwa anthu onyada.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

뉴스레터 구독

새로운 프로필과 행사, 플랫폼 소식을 받아 보세요.