Masalimo 125

Amene amadalira Yehova ali ngati phiri la Ziyoni, limene silingagwedezeke koma ndi lokhala mpaka muyaya. Monga mapiri azungulira Yerusalemu, momwemonso Yehova azungulira anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya. Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama, kuti anthu olungamawo angachite nawonso zoyipa. Yehova chitirani zabwino amene ndi abwino, amene ndi olungama mtima Koma amene amatembenukira ku njira zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi anthu ochita zoyipa. Mtendere ukhale pa Israeli.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

뉴스레터 구독

새로운 프로필과 행사, 플랫폼 소식을 받아 보세요.