Masalimo 142

Ndikulirira Yehova mofuwula; ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo. Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake; ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake. Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga, ndinu amene mudziwa njira yanga. Mʼnjira imene ndimayendamo anthu anditchera msampha mobisa. Yangʼanani kumanja kwanga ndipo onani; palibe amene akukhudzika nane. Ndilibe pothawira; palibe amene amasamala za moyo wanga. Ndilirira Inu Yehova; ndikuti, “Ndinu pothawirapo panga, gawo langa mʼdziko la anthu amoyo.” Mverani kulira kwanga pakuti ndathedwa nzeru; pulumutseni kwa amene akundithamangitsa pakuti ndi amphamvu kuposa ine. Tulutseni mʼndende yanga kuti nditamande dzina lanu. Ndipo anthu olungama adzandizungulira chifukwa cha zabwino zanu pa ine.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

Unseren Newsletter abonnieren

Bleiben Sie über neue Profile, Veranstaltungen und Plattform-Updates informiert.