Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi.Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.Ogi mfumu ya mzinda wa Basani, amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi.Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo.Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:mfumu ya Yeriko imodzi mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli imodzimfumu ya Yerusalemu imodzi mfumu ya Hebroni imodzimfumu ya Yarimuti imodzi mfumu ya Lakisi imodzimfumu ya Egiloni imodzi mfumu ya Gezeri imodzimfumu ya Debri imodzi mfumu ya Gederi imodzimfumu ya Horima imodzi mfumu ya Aradi imodzimfumu ya Libina imodzi mfumu ya Adulamu imodzimfumu ya Makeda imodzi mfumu ya Beteli imodzimfumu ya Tapuwa imodzi mfumu ya Heferi imodzimfumu ya Afeki imodzi mfumu ya Lasaroni imodzimfumu ya Madoni imodzi mfumu ya Hazori imodzimfumu ya Simuroni Meroni imodzi mfumu ya Akisafu imodzimfumu ya Taanaki imodzi mfumu ya Megido imodzimfumu ya Kadesi imodzi mfumu ya Yokineamu ku Karimeli imodzimfumu ya Dori ku Nafoti Dori imodzi mfumu ya Goyini ku Giligala imodzimfumu ya Tiriza imodzi mafumu onse pamodzi analipo 31.