Hoseya 3

Yehova anati kwa ine, “Pita kamukondenso mkazi wako, ngakhale ali pa chibwenzi ndi wina ndi kuti ndi wachigololo. Mukonde iyeyo monga momwe Yehova amakondera Aisraeli, ngakhale iwo amapita kukapembedza milungu ina ndi kukonda nsembe za keke zamphesa zowuma.” Motero ndinamukwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iwiri ya barele. Kenaka ndinamuwuza mkaziyo kuti, “Ukhale nane masiku ambiri; usachitenso zachiwerewere kapena chigololo ndi munthu wina, ndipo ine ndidzakhala nawe.” Pakuti Aisraeli adzakhala masiku ambiri opanda mfumu kapena kalonga, osapereka nsembe kapena kuyimika miyala yachipembedzo, wopanda efodi kapena fano. Pambuyo pake Aisraeli adzabwerera ndi kufunafuna Yehova Mulungu wawo ndi Davide mfumu yawo. Adzabwera kwa Yehova akunjenjemera ndipo adzalandira madalitso mʼmasiku awo otsiriza.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

뉴스레터 구독

새로운 프로필과 행사, 플랫폼 소식을 받아 보세요.