Masalimo 53

Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino. Mulungu kumwamba amayangʼana pansi pano pa ana a anthu kuti aone ngati alipo wina wanzeru, wofunafuna Mulungu. Aliyense wabwerera, iwo onse pamodzi akhala oyipa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino, ngakhale mmodzi. Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi; anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi, ndipo sapemphera kwa Mulungu? Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu pamene panalibe kanthu kochititsa mantha. Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo; inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza. Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni! Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake, lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

Subscribe to our newsletter

Stay updated with new profiles, events, and platform updates.