Masalimo 87

Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera; Yehova amakonda zipata za Ziyoni kupambana malo onse okhalamo a Yakobo. Za ulemerero wako zimakambidwa, Iwe mzinda wa Mulungu: Sela “Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ” Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti, “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye, ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.” Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” Sela Oyimba ndi ovina omwe adzati, “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

Подписаться на нашу рассылку

Следите за новыми профилями, мероприятиями и обновлениями платформы.