Masalimo 100

Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Mulambireni Yehova mosangalala; bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero. Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake. Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko ndi ku mabwalo ake ndi matamando; muyamikeni ndi kutamanda dzina lake. Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya; kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

Assinar nossa newsletter

Mantenha-se a par dos novos perfis, eventos e novidades da plataforma.