Masalimo 120

Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga, ndipo Iye amandiyankha. Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza, ndi kwa anthu achinyengo. Kodi adzakuchitani chiyani, ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo? Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo, ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya. Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki, kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara! Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati pa iwo amene amadana ndi mtendere. Ine ndine munthu wamtendere; koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.

Buku Lopatulika (Chichewa)

copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc — CC-BY-SA-4.0 — CC-BY-SA-4.0

Suscribirse a nuestro boletín

Manténgase al día de los nuevos perfiles, eventos y novedades de la plataforma.